Ndikuti ndikakhala chete
Kulingalila kodi mdalakwanji ine chauta?
Mafunso mngochuluka,
Ndidalakwanji mphambe kuti
Mundisiye ndekha ine?
Uko kumasamba aku Mdekela,
Pomwe padagona gogo Yosiya,
Pomwetu pali gogo Ndau
M'chimwene wanga ali mtulo,
Ndatani ine namalenga?
Misozi ndiyosatha,
Tidali awiri dzana lero ndili ndekha.
Ndatsala ndekha chauta,
Uko kumasamba akwa Kaludzu,
Mchimwene ali gone,ekhaekha
Mwandilnga kokwana chata,ndikhululukileni,
Ndine mwanu ngati enawa
Chonde mulungu wanga..
Mwandisiya ndekha mthengo!!
Taonani chauta kumbuyo kwangaku,
Zopinga mzambiri inu mphambe,
Ndiri ndekha mkachipinda kanga chiuta,
Mngotani moyo kusautsa chotere chauta?
Khululukileni ine,
Potitu mngochuluka ondilondalonda
Ndatsala ndekhatu atate,
Tetezeni ine,mwana wanu..
No comments:
Post a Comment